Davide apempha Mulungu amlanditse
Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto. Cilangizo ca Davide. Muja Azift anamuka nauza Sauli, kuti, Kodi Davide sabisala kwathu nanga?
1 Ndipulumutseni, Mulungu, mwa dzina lanu,
Ndipo mundiweruze ndi mphamvuyanu.
2 Imvani pemphero langa, Mulungu;
Cherani khutu mau a pakamwa panga.
3 Pakuti alendo andiukira,
Ndipo oopsa afunafuna moyo wanga;
Sadziikira Mulungu pamaso pao.
4 Taonani, Mulungu ndiye mthandizi wanga:
Ambuye ndiye wacirikiza moyo wanga.
5 Adzabwezera coipa adani anga:
Aduleni m’coonadi canu.
6 Ine mwini ndidzapereka nsembe kwa Inu:
Ndidzayamika dzina lanu, Yehova, pakuti nlokoma.
7 Pakuti anandilanditsa m’nsautso yonse;
Ndipo ndapenya ndi diso langa ico ndakhumbira pa adani anga,