Masalmo 53

Kupusa ndi kuipa kwa anthu

Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Mahalat. Cilanidzo ca Davide.

1 Citsiru cimati mumtima mwace, Kulibe Mulungu.

Acita zobvunda, acita cosalungama conyansa;

Kulibe wakucita bwino.

2 Mulungu m’mwamba anaweramira pa ana a anthu,

Kuti aone ngati aliko wanzeru, Wakufuna Mulungu.

3 Onse anabwerera; anabvunda mtima pamodzi;

Palibe mmodzi wakucita bwino, nnena mmodzi.

4 Kodi ocita zopanda pace sadziwa?

Pomadya anthu anga monga akudya mkate;

Ndipo saitana Mulungu.

5 Pamenepo anaopa kwakukuru, popanda cifukwa ca kuopa:

Pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe;

Unawacititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.

6 Ha, cipulumutso ca Israyeli cicokere m’Ziyoni!

Pakubweretsa Mulungu anthu ace a m’ndende,

Yakobo adzakondwera, Israyeli adzasekera.