Masalmo 48

Ukoma ndi ulemerero wa Ziyoni

Nyimbo; Salmo la ana a Kora.

1 Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi,

M’mudzi wa Mulungu wathu, m’phiri lace loyera.

2 Phiri la Ziyoni, cikhalidwe cace ncokoma

Ku mbali zace za kumpoto,

Ndilo cimwemwe ca dziko lonse lapansi,

Mudzi wa mfumu yaikuru.

3 Mulungu adziwika m’zinyumba zace ngati msanje.

4 Pakuti, taonani, mafumuwo anasonkhana,

Anapitira pamodzi.

5 Anapenya mudziwo, ndipo pamenepo anadabwa;

Anaopsedwa, nathawako.

6 Pomwepo anagwidwa nako kunthunthumira;

Anamva cowawa, ngati wam’cikuta.

7 Muswa zombo za ku Tarisi ndi mphepo ya kum’mawa.

8 Monga tidamva, momwemo tidapenya

M’mudzi wa Yehova wa makamu, m’mudzi wa Mulungu wathu:

Mulungu adzaukhazikitsa ku nthawi yamuyaya.

9 Tidalingalira za cifundo canu, Mulungu,

M’kati mwa Kacisi wanu.

10 Monga dzina lanu, Mulungu,

Momwemo lemekezo lanu ku malekezero a dziko lapansi:

M’dzanja lamanja lanu mudzala cilungamo.

11 Likondwere phiri la Ziyoni,

Asekere ana akazi a Yuda,

Cifukwa ca maweruzo anu.

12 Zungulirani Ziyoni, ndipo muuzinge;

Werengani nsanja zace.

13 Penyetsetsani malinga ace,

Yesetsani zinyumba zace;

Kuti mukaziwerengere mibadwo ikudza m’mbuyo.

14 Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu ku nthawi za nthawi:

Adzatitsogolera kufikira imfa.