Mau a kulemekeza Mulungu mwini dziko lonse lapansi
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salmo la ana a Koro.
1 Ombani m’manja, mitundu yonse ya anthu;
Pfuulirani kwa Mulungu ndi liu la kuyimbitsa.
2 Pakuti Yehova Wam’mwambamwamba ndiye woopsa;
Ndiye mfumu yaikuru pa dziko lonse lapansi.
3 Atigonjetsera anthu,
Naika amitundu pansi pa mapazi athu.
4 Atisankhira colowa cathu,
Cokometsetsa ca Yakobo amene anamkonda.
5 Mulungu wakwera ndi mpfuu,
Yehova ndi liu la lipenga.
6 Yimbirani Mulungu, yimbirani;
Yimbirani Mfumu yathu, yimbirani.
7 Pakuti Mulungu ndiye Mfumu ya dziko lonse lapansi;
Yimbirani ndi cilangizo.
8 Mulungu ndiye Mfumu ya amitundu:
Mulungu akhala pa mpando wacifumu wace woyera.
9 Akulu a anthu asonkhana
Akhale anthu a Mulungu wa Abrahamu:
Pakuti zikopa za dziko lapansi nza Mulungu;
Akwezeka kwakukuru Iyeyo.