Mulungu ndiye pothawirapo anthu ace
Kwa Mkulu wa Nyimbo; Cilangizo ca kwa ana a Kora. Pa Alamot. Nyimbo.
1 Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu,
Thandizo lopezekeratu m’masautso.
2 Cifukwa cace sitidzacita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi,
Angakhale mapiri asunthika, nakhala m’kati mwa nyanja;
3 Cinkana madzi ace akokoma, nacita thobvu,
Nagwedezeka mapiri ndi kudzala kwace.
4 Pali mtsinje, ngalande zace zidzakondweretsa mudzi wa Mulungu.
Malo oyera okhalamo Wam’mwambamwamba,
5 Mulungu ali m’kati mwace, sudzasunthika:
Mulungu adzauthandiza mbanda kuca.
6 Amitundu anapokosera; maufumu anagwedezeka:
Ananena mau, dziko lapansi linasungunuka.
7 Yehova wa makamu ali ndi ife;
Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.
8 Idzani, penyani nchito za Yehova,
Amene acita zopululutsa pa dziko lapansi.
9 Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi;
Athyola uta, nadula nthungo;
Atentha magareta ndi moto.
10 Khalani cete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu:
Ndidzabuka mwa amitundu,
Ndidzabuka pa dziko lapansi.
11 Yehova wa makamu ali ndi ife,
Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu,