Mtima wolira kuyanjana ndi Mulungu m’Kacisi
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Cilangizo ca kwa ana a Kora.
1 Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje;
Motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.
2 Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu, la kwa Mulungu wamoyo:
Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?
3 Misozi yanga yakhalangati cakudya canga,
Usana ndi usiku;
Pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse,
Mulungu wako ali kuti?
4 Ndizikumbukila izi ndipo nditsanulira moyo wanga m’kati mwa ine,
Pakuti ndidafopita ndi unyinji wa anthu,
Ndinawatsogolera ku nyumba ya Mulungu, ndi mau akuyimbitsa ndi kuyamika,
Ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.
5 Udziweramiranji moyo wanga iwe?
Ndi kuzingwa m’kati mwanga?
Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso
Cifukwa ca cipulumutso ca nkhope yace.
6 Mulungu wanga, moyo wanga
Udziweramira m’kati mwanga;
Cifukwa cace ndikumbukila Inu m’dziko la Yordano,
Ndi mu Ahermone, m’kaphiri ka Mizara.
7 Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya,
Pa mkokomo wa matiti anu: Mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine.
8 Koma usana Yehova adzalamulira cifundo cace,
Ndipo usiku Nyimbo yace idzakhala ndi ine.
Inde pemphero la kwa Yehova wa moyowanga.
9 Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa, mwandiiwala cifukwa ninji?
Ndimayenderanji wakulira Cifukwa ca kundipsinja mdaniyo?
10 Adani anga andinyoza ndi kundityola mafupa anga;
Pakunena ndine dzuwa lonse,
Mulungu wako ali kuti?
11 Udziweramiranji moyo wanga iwe?
Ndi kuzingwa m’kati mwanga?
Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso,
Ndiye cipulumutso ca nkhope yanga ndi Mulungu wanga,