Kupepuka kwa moyo uno
Kwa Mkulu wa Nyimbo, kwa Yedutun, Salmo la Davide.
1 Ndinati, Ndidzasunga njira zanga,
Kuti ndingacimwe ndi lilime langa:
Ndidzasunga pakamwa panga ndi cam’kamwa,
Pokhala woipa ali pamaso panga.
2 Ndinatonthola osanena mau, ndinakhala cete osalawa cokoma;
Ndipo cisoni canga cinabuka.
3 Mtima wanga unatentha m’kati mwaine;
Unayaka moto pakulingirira ine:
Pamenepo ndinalankhula ndi lilime langa:
4 Yehova, mundidziwitse cimariziro canga,
Ndi mawerengedwe a masiku anga ndi angati;
Ndidziwe malekezero anga,
5 Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja;
Ndipo zaka zanga ziri ngati cabe pamaso panu:
Indedi munthu ali yense angakhale wokhazikika, ali cabe konse.
6 Indedi munthu ayenda ngati mthunzi:
Indedi abvutika cabe:
Asonkhanitsa cuma, ndipo sadziwa adzacilandira ndani?
7 Ndipo tsopano, Ambuye, ndilindira ciani?
Ciyembekezo canga ciri pa Inu.
8 Ndipulumutseni kwa zolakwa zangazonse:
Musandiike ndikhale cotonza ca wopusa.
9 Ndinakhala du, sindinatsegula pakamwa panga;
Cifukwa inu mudacicita.
10 Mundicotsere cobvutitsa canu;
Pandithera ine cifukwa ca kulanga kwa dzanja lanu.
11 Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula cifukwa ca mphulupulu,
Mukanganula kukongola kwace monga mumacita ndi kadzoce:
Indedi, munthu ali yense ali cabe.
12 Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo cherani khutu kulira kwanga;
Musakhale cete pa misozi yanga:
Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu,
Wosakhazikika, monga makolo anga onse.
13 Ndiloleni, kuti nditsitsimuke,
Ndisanamuke ndi kukhala kuli zi.