Masalmo 38

Davide aulula zoipa zace, apempha Mulungu amkhululukire namthandize

Salmo la Davtde, lakukumbutsa.

1 Yehova, musandidzudzule ndi mkwiyo wanu:

Ndipo musandilange moopsa m’mtima mwanu.

2 Pakuti mibvi yanu yandilowa,

Ndi dzanja lanu landigwera.

3 Mumnofu mwanga mulibe camoyo cifukwa ca ukali wanu;

Ndipo m’mafupa anga simuzizira, cifukwa ca colakwa canga.

4 Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga:

Ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera.

5 Mabala anga anunkha, adaola, Cifukwa ca kupusa kwanga.

6 Ndapindika, ndawerama kwakukuru;

Ndimayenda woliralira tsiku lonse.

7 Pakuti m’cuuno mwanga mutentha kwambiri;

Palibe pamoyo m’mnofu mwanga,

8 Ndafoka ine, ndipo ndacinjizidwa:

Ndabangula cifukwa ca kumyuka mtima wanga.

9 Ambuye, cikhumbo canga conse ciri pamaso panu;

Ndipo kubuula kwanga sikubisika kwa Inu.

10 Mtima wanga ugundagunda, mphamvu yanga yacoka:

Ndipo kuunika kwa maso anga, ndi iko komwe kwandicokera.

11 Ondikonda ndi anzanga apewa mliri wanga;

Ndipo anansi anga aima patali.

12 Ndipo andichera misampha iwo akufuna moyo wanga;

Ndipo iwo akuyesa kundicitira coipa alankhula zoononga,

Nalingirira zonyenga tsiku lonse.

13 Koma ine, monga gonthi, sindimva;

Ndipo monga munthu wosalankhula, sinditsegula pakamwa panga.

14 Inde ndikunga munthu wosamva,

Ndipo m’kamwa mwanga mulibe makani.

15 Pakuti ndikuyembekezani Inu, Yehova;

Inu mudzayankha, Ambuye Mulungu wanga.

16 Pakuti ndinati, Asakondwerere ine:

Pakuterereka phazi langa, asadzikuze pa ine.

17 Ndafikana potsimphina;

Ndipo cisoni canga ciri pamaso panga cikhalire.

18 Pakuti ndidzafotokozera mphulupulu yanga;

Nditenga nkhawa cifukwa ca chimo langa.

19 Koma adani anga ali ndi moyo, nakhalandi mphamvu:

Ndipo akundida kopanda cifukwa acuruka.

20 Ndipo iwo akubwezera coipa pa cabwino

Atsutsana nane, popeza nditsata cabwino.

21 Musanditaye, Yehova:

Mulungu wanga, musakhale kutali ndi ine.

22 Fulumirani kundithandiza,

Ambuye, cipulumutso canga.