Masalmo 36

Kuipitsitsa kwa anthu, kukometsetsa kwa Mulungu

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova.

1 Colakwa ca woipayo cimati m’kati mwa mtima wanga,

Palibe kuopa Mulungu pamaso pace.

2 Pakud adzidyoletsa yekha m’kuona kwace,

Kuti anthu sadzacipeza coipa cace ndi kukwiya naco.

3 Mau a pakamwa pace ndiwo opanda pace ndi onyenga:

Waleka kuzindikira ndi kucita bwino.

4 Alingirira zopanda pace pakama pace;

Adziika panjira posad pabwino;

Coipa saipidwa naco.

5 Yehova, m’mwambamuli cifundo canu;

Coonadi canu cifikira kuthambo.

6 Cilungamo canu cikunga mapiri a Mulungu;

Maweruzo anu akunga cozama cacikuru:

Yehova, musunga munthu ndi nyama.

7 Ha! cifundo canu, Mulungu, ncokondedwadi!

Ndipo ana a anthu athawira ku mthunzi wa mapiko anu.

8 Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m’nyumba mwanu:

Ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu.

9 Pakuti citsime ca moyo ciri ndi Inu:

M’kuunika kwanu tidzaona kuunika.

10 Tanimphitsani cifundo canu pa iwo akudziwa Inu;

Ndi cilungamo canu pa oongoka mtima.

11 Phazi la akudzikuza lisandifikire ine,

Ndi dzanja la oipa lisandicotse.

12 Pomwepo padagwera ocita zopanda pace:

Anawalikha, ndipo sadzatha kuukanso.