Mwai wa munthu amene Mulungu wamkhululukira
Cilangizo ca Davide.
1 Wodala munthuyo wokhululukidwa chimo lace;
Wokwiriridwa coipa cace.
2 Wodala munthuyu Yehova samwerengera mphulupulu zace;
Ndimo mumzimu mwace mulibe cinyengo.
3 Pamene ndinakhala cete mafupa anga anakalamba
Ndi kubuula kwanga tsiku lonse.
4 Cifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine;
Uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.
5 Ndinabvomera coipa canga kwa Inu;
Ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa.
Ndinati, Ndidzaululira Yehova macimo anga;
Ndipo munakhululukira coipa ca kulakwa kwanga.
6 Cifukwa cace oyera mtima onse apemphere kwa Inu,
Pa nthawi ya kupeza Inu:
Indetu pakusefuka madzi akuru
Sadzamfikira iye.
7 Inu ndinu mobisalira mwanga; M’nsautso mudzandisunga;
Mudzandizinga ndi Nyimbo za cipulumutso.
8 Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo;
Ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.
9 Musakhale monga kavalo, kapena ngati buru, wopanda nzeru:
Zomangira zao ndizo cam’kamwa ndi capamutu zakuwakokera,
Pakuti ukapanda kutero sadzakuyandikiza.
10 Zisoni zambiri zigwera woipa:
Koma cifundo cidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova.
11 Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima;
Ndipo pfuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.