Kukhulupirika kwa Mulungu
Salimo la Davide, muja anathawa Abisalomu mwana wace.
1 Yehova! Ha! acuruka nanga akundisautsa ine!
Akundiukira ine ndi ambiri.
2 Ambiri amati kwa moyo wanga,
Alibe cipulumutso mwa Mulungu.
3 Ndipo Inu Yehova, ndinu cikopa canga;
Ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.
4 Ndipfuula kwa Yehova ndi mau anga,
Ndipo andiyankha m’phiri lace loyera,
5 Ndinagona ine pansi, ndinagona tulo;
Ndinauka; pakuti Yehova anandicirikiza.
6 Sindidzaopa unyinji wa anthu akundizinga ine.
7 Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga!
Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya;
Mwawatyola mano oipawo.
8 Cipulumutso nca Yehova;
Dalitso lanu likhale pa anthu anu.