Acenjeza akuru alemekeze Mulungu
Salmo la Davide.
1 Perekani kwa Yehova, inu ana a amphamvu,
Perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
2 Perekani kwa Yehova ulemerero wa dzina lace:
Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa.
3 Liu la Yehova liri pamadzi;
Mulungu wa ulemerero agunda,
Ndiye Yehova pa madzi ambiri.
4 Liu la Yehova ndi lamphamvu;
Liu la Yehova ndi lalikurukuru.
5 Liu la Yehova lithyola mitengo yamkungudza;
Inde Yehova athyola mikungudza ya ku Lebano.
6 Aitumphitsa monga mwana wa ng’ombe;
Lebano ndi Sirio monga msona wa njati.
7 Liu la Yehova ligawa malawi a moto.
8 Liu la Yehova ligwedeza cipululu;
Yehova agwedeza cipululu ca Kadese.
9 Liu la Yehova liswetsa nyama zazikazi,
Ndipo lipulula nkhalango:
Ndipo m’Kacisi mwace zonse ziri m’mwemo zimati, Ulemerero:
10 Yehova anakhala pa Cigumula:
Inde Yehova akhala mfumu ku nthawi yomka muyaya.
11 Yehova adzapatsa anthu ace mphamvu:
Yehova adzadalitsa anthu ace ndi mtendere.