Apempha cipulumutso, ayamika populumutsidwa
Salmo la Davide.
1 Kwa Inu, Yehova, ndidzapfuulira;
Thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva:
Pakuti ngati munditontholera ine,
Ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.
2 Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu,
Pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.
3 Musandikoke kundicotsa pamodzi ndi oipa,
Ndi ocita zopanda pace;
Amene alankhula zamtendere ndi anansi ao,
Koma mumtima mwao muli coipa.
4 Muwapatse monga mwa nchito zao, ndi monga mwa coipa cocita iwo:
Muwapatse monga mwa macitidwe a manja ao;
Muwabwezere zoyenera iwo.
5 Pakuti sasamala nchito za Yehova,
Kapena macitidwe a manja ace,
Adzawapasula, osawamanganso.
6 Wodalitsika Yehova,
Pakuti adamva mau a kupemba kwanga.
7 Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi cikopa canga;
Mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza:
Cifukwa cace mtima wanga ukondwera kwakukuru;
Ndipo ndidzamyamika nayo Nyimbo yanga.
8 Yehova ndiye mphamvu yao,
Inde mphamvu ya cipulumutso ca wodzozedwa wace.
9 Pulumutsani anthu anu, ndi kudalitsa colandira canu:
Muwawetenso, ndi kuwanyamula nthawi zonse.