Davide popempha Mulungu amweruze, achula zokoma zace
Salmo la Davide.
1 Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda m’ungwiro wanga:
Ndipo ndakhulupirira Yehova, sindidzaterereka.
2 Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe;
Yeretsani imso zanga ndi mtima wanga.
3 Pakuti cifundo canu ciri pamaso panga;
Ndipo ndayenda m’coona canu.
4 Sindinakhala pansi ndi anthu acabe;
Kapena kutsagana nao anthu otyasika.
5 Ndidana nao msonkhano wa ocimwa,
Ndipo sindidzakhala nao pansi ocita zoipa.
6 Ndidzasamba manja anga mosalakwa;
Kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova:
7 Kuti ndimveketse mau a ciyamiko,
Ndi kulalikira nchito zanu zonse zozizwa.
8 Yehova, ndikonda cikhalidwe ca nyumba yanu,
Ndi malo akukhalamo ulemerero wanu.
9 Musandicotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa,
Kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi:
10 Amene m’manja mwao muli mphulupulu,
Ndi dzanja lao lamanja ladzala ndi zokometsera mlandu.
11 Koma ine, ndidzayenda m’ungwiro wanga;
Mundiombole, ndipo ndicitireni cifundo.
12 Phazi langa liponda pacidikha:
M’masonkhano ndidzalemekeza Yehova.