Amwai amene Yehova akhala Mbusa wao
Salimo la Davide,
1 Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa.
2 Andigonetsa ku busa lamsipu:
Anditsogolera ku madzi ndikha.
3 Atsitsimutsa moyo wanga;
Anditsogolera m’mabande a cilungamo, cifukwa ca dzina lace.
4 Inde, ndingakhale ndiyenda m’cigwa ca mthunzi wa Imfa,
Sindidzaopa coipa; pakuti Inu muli ndi ine:
Cibonga canu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine,
5 Mundiyalikira gome pamaso panga m’kuona kwa adani anga:
Mwandidzoza mutu wanga mafuta; cikho canga cisefuka.
6 Inde ukoma ndi cifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga:
Ndipo ndidzakhala m’nyumba ya Yehova masiku onse.