Kupempherera mfumu poturukira iye kunkhondo
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salmo la Davide.
1 Yehova akubvomereze tsiku la nsautso;
Dzina la Mulungu wa Yakobo likuike pamsanje;
2 Likutumizire thandizo loturuka m’malo oyera,
Ndipo likugwirizize kucokera m’Ziyoni;
3 Likumbukile zopereka zako zonse,
Lilandire nsembe yako yopsereza;
4 Likupatse ca mtima wako,
Ndipo likwaniritse upo wako wonse.
5 Tidzapfuula mokondwera mwa cipulumutso canu,
Ndipo m’dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera:
Yehova akwaniritse mapempho ako onse.
6 Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wace;
Adzambvomereza m’Mwamba mwace moyera
Ndi mphamvu ya cipulumutso ca dzanja lace lamanja.
7 Ena atama magareca, ndi ena akavalo:
Koma ife tidzachula dzina la Yehova Mulungu wathu.
8 Iwowa anagonieka, nagwa:
Koma ife tauka, ndipo takhala ciriri.
9 Yehova, pulumutsani,
Mfumuyo atibvomereze tsiku lakuitana ife.