Davide apempha Mulungu amsunge pa ofuna kumuononga
Pemphero la Davide.
1 Yehova, imvani cilungamo, mverani mpfuu wanga;
Cherani khutu ku pemphero langa losaturuka m’milomo ya cinyengo,
2 Pankhope panu paturuke ciweruzo canga;
Maso anu apenyerere zolunjika,
3 Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku;
Mwandisuntha, simupeza kanthu;
Ndatsimikiza mtima kuti m’kamwa mwanga simudzalakwa.
4 Za macitidwe a anthu, ndaceniera ndi mau a milomo yanu
Ndingalowe njira za woononga.
5 M’mayendedwe anga ndasunga mabande anu,
Mapazi anga sanaterereka.
6 Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu:
Cherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga.
7 Onetsani cifundo canu codabwiza, Inu wakupulumutsa okhulupirira Inu
Kwa iwo akuwaukira ndi dzanja lanu lamanja.
8 Ndisungeni monga kamwana ka m’diso,
Ndifungatireni mu mthunzi wa mapiko anu,
9 Kundilanditsa kwa oipa amene andipasula,
Adani a pa moyo wanga amene andizinga.
10 Mafuta ao awatsekereza;
M’kamwa mwao alankhula modzikuza.
11 Tsopano anatizinga m’mayendedwe athu:
Apenyetsetsa m’maso kuti atigwetse pansi.
12 Afanana ndi mkango wofuna kumwetula,
Ndi msona wa mkango wakukhala mobisalamo.
13 Ukani Yehova,
Mumtsekereze, mumgwetse:
Landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu;
14 Kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova,
Kwa anthu a dziko lapansi pano amene colowa cao ciri m’moyo uno,
Ndipo mimba yao muidzaza ndi cuma canu cobisika:
Akhuta mtima ndi ana,
Nasiyira ana amakanda zocuruka zao.
15 Koma ine ndidzapenyerera nkhope yanu m’cilungamo:
Ndidzakhuta mtima ndi maonekedwe anu, pamene ndidzauka.