Cikhalidwe ca munthu woona wa Mulungu
Salmo la Davide.
1 Yehova, ndani adzagonera m’cihema mwanu?
Adzagonera ndani m’phiri lanu lopatulika?
2 Iye wakuyendayo mokwanira, nacita cilungamo,
Nanena zoonadi mumtima mwace.
3 Amene sasinjirira ndi lilime lace,
Sacitira mnzace coipa,
Ndipo satola msece pa mnansi wace.
4 M’maso mwace munthu woonongeka anyozeka;
Koma awacitira ulemu akuopa Yehova.
Atalumbira kwa tsoka lace, sasintha ai.
5 Ndarama zace sakongoletsa mofuna phindu lalikuru,
Ndipo salandira cokometsera mlandu kutsutsa wosacimwa.
Munthu wakucita izi sadzagwedezeka ku nthawi zonse,