Kudandaula kwa Ayuda ku Babulo
1 Ku mitsinje ya ku Babulo,
Kumeneko tinakhala pansi, inde tinalira,
Pokumbukila Ziyoni.
2 Pa msondodzi uli m’mwemo Tinapacika mazeze athu.
3 Popeza pamenepo akutigwirawo anatifunsa nyimbo,
Ndipo akutizunza anafuna tisekere,
Ndi kuti, Mutiyimbire nyimbo imodzi ya ku Ziyoni.
4 Tidati, Tidzayimba bwanji nyimbo ya Yehova
M’dziko lacilendo?
5 Ndikakuiwalani, Yerusalemu,
Dzanja lamanja langa liiwale luso lace.
6 Lilime langa limamatike ku nsaya zanga,
Ndikapanda kukumbukila inu;
Ndikapanda kusankha Yerusalemu
Koposa cimwemwe canga copambana.
7 Yehova, kumbukilani ana a Edomu
Tsiku la Yerusalemu;
Amene adati, Gamulani, gamulani,
Kufikira maziko ace.
8 Mwana wamkazi wa ku Babulo, iwe amene udzapasulidwa;
Wodala iye amene adzakubwezera cilango
Monga umo unaticitira ife.
9 Wodala iye amene adzagwira makanda ako,
Ndi kuwaphwanya pathanthwe.