Mulungu alemekezedwa pa ukulu wace. Mafano ndi acabe
1 Haleluya;
Lemekezani dzina la Yehova;
Lemekezani inu atumiki a Yehova:
2 Inu akuimirira m’nyumba ya Yehova,
M’mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.
3 Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino;
Muyimbire zolemekeza dzina lace; pakuti nkokondweretsa kutero.
4 Pakuti Yehova anadzisankhira Yakobo,
Israyeli, akhale cuma cace ceni ceni.
5 Pakuti ndidziwa kuti Yehova ndi wamkuru,
Ndi Ambuye wathu aposa milungu yonse.
6 Ciri conse cimkonda Yehova acicita,
Kumwamba ndi pa dziko lapansi, m’nyanja ndi mozama monse.
7 Akweza mitambo icokere ku malekezero a dziko lapansi;
Ang’animitsa mphezi zidzetse mvula;
Aturutsa mphepo mosungira mwace.
8 Anapanda oyamba a Aigupto,
Kuyambira munthu kufikira zoweta.
9 Anatumiza zizindikilo ndi zodabwiza pakati pako,
Aigupto iwe, Pa Farao ndi pa omtumikira onse.
10 Ndiye amene anapanda amitundu ambiri.
Napha mafumu amphamvu;
11 Sihoni mfumu ya Aamori,
Ndi Ogi mfumu ya Basana,
Ndi maufumu onse a Kanani:
12 Ndipo anapereka dziko lao likhale cosiyira,
Cosiyira ca kwa Israyeli anthu ace.
13 Dzina lanu, Yehova, likhala kosatha;
Cikumbukilo canu, Yehova, kufikira mibadwo mibadwo.
14 Pakuti Yehova adzaweruza anthu ace,
Koma adzaleka atumiki ace.
15 Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golidi,
Nchito ya manja a anthu.
16 Pakamwa ali napo koma osalankhula;
Maso ali nao, koma osapenya;
17 Makutu ali nao, koma osamva;
Inde, pakamwa pao palibe mpweya.
18 Akuwapanga adzafanana nao;
Inde, onse akuwakhulupirira.
19 A nyumba ya Israyeli inu, lemekezani Yehova:
A nyumba ya Aroni inu, lemekezani Yehova:
20 A nyumba ya Levi inu, lemekezani Yehova:
Inu akuopa Yehova, lemekezani Yehova.
21 Alemekezedwe Yehova kucokera m’Ziyoni,
Amene akhala m’Yerusalemu.
Haleluya,