Cikondano ca abale ndi cokoma
Nyimbo yokwerera; ya Davide.
1 Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu
Kuti abale akhale pamodzi!
2 Ndiko ngati mafuta a mtengo wace pamutu,
Akutsikira ku ndebvu,
Inde ku ndebvu za Aroni;
Akutsikira ku mkawo wa zobvala zace
3 Ngati mame a ku Hermoni,
Akutsikira pa mapiri a Ziyoni:
Pakuti pamenepo Yehova analamulira dalitsolo,
Ndilo moyo womka muyaya,