Masalmo 131

Kudzicepetsa kwa Davide pakupemphera

Nyimbo yokwerera, ya Davide.

1 Yehova, mtima wanga sunadzikuza

Ndi maso anga sanakwezeka;

Ndipo sindinatsata zazikuru,

Kapena zodabwiza zondiposa.

2 Indedi, ndinalinganiza ndi kutontholetsa moyo wanga;

Ngati mwana womletsa kuyamwa amace,

Moyo wanga ndiri nao ngati mwana womletsa kuyamwa.

3 Israyeli, uyembekezere Yehova,

Kuyambira tsopano kufikira kosatha.