Munkhawa athawira Mulungu namkhulupirira
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salmo la Davide.
1 Mudzandiiwala ciiwalire, Yehova, kufikira liti?
Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti?
2 Ndidzacita uphungu m’moyo mwanga kufikira liti,
Pokhala ndi cisoni m’mtima mwanga tsiku lonse?
Adzandiukira ine mdani wanga kufikira liti?
3 Penyani, ndiyankheni, Yehova Mulungu wanga:
Penyetsani maso anga, kuti ndingagone tulo ta imfa;
4 Kuti anganene mdani wanga, Ndamlaka;
Ndipo angakondwere otsutsana nane posunthika ine.
5 Koma ine ndakhulupira pa cifundo canu;
Mtima wanga udzakondwera naco cipulumutso canu:
6 Ndidzayimbira Yehova,
Pakuti anandicitira zokoma.