Israyeli asautsidwa koma osafafanizidwa
Nyimbo yokwerera.
1 Anandisautsa kawiri kawiri kuyambira ubwana wanga,
Anene tsono Israyeli;
2 Anandisautsa kawiri kawiri kuyambira ubwana wanga;
Koma sanandilaka.
3 Olima analima pamsana panga;
Anatalikitsa mipere yao.
4 Yehova ndiye wolungama;
Anadulatu zingwe za oipa.
5 Acite manyazi nabwerere m’mbuyo.
Onse akudana naye Ziyoni.
6 Akhale ngati udzu womera patsindwi,
Wakufota asanauzule;
7 Umene womweta sadzaza nao dzanja lace,
Kapena womanga mitolo sakupatira manja.
8 Angakhale opitirirapo sanena,
Dalitso la Mulungu likhale pa inu;
Tikudalitsani m’dzina la Yehova.