Wakuopa Yehova adalitsidwa m’banja mwace
Nyimbo yokwerera.
1 Wodala yense wakuopa Yehova, Wakuyenda m’njira zace.
2 Pakuti udzadya za nchito ya manja ako;
Wodala iwe, ndipo kudzakukomera.
3 Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m’mbali za nyumba yako;
Ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako.
4 Taonani, m’mwemo adzadalitsika
Munthu wakuopa Yehova.
5 Yehova adzakudalitsa ali m’Ziyoni
Ndipo udzaona zokoma za Yerusalemu masiku onse a moyo wako.
6 Inde, udzaona zidzukulu zako.
Mtendere ukhale ndi Israyeli.