Mulungu yekha walanditsa anthu ace
Nyimbo vokwerera: ya Davide,
1 Akadapanda kukhala nafe Yehova,
Anene tsono Israyeli;
2 Akadapanda kukhala nafe Yehova,
Pakutiukira anthu:
3 Akadatimeza amoyo,
Potipsera mtima wao.
4 Akadatimiza madziwo,
Mtsinje ukadapita pa moyo wathu;
5 Madzi odzikuza akadapita pa moyo wathu.
6 Alemekezedwe Yehova,
Amene sanatipereka kumano kwao tikhale cakudya cao.
7 Moyo wathu unaonjoka ngati mbalame mu msampha wa msodzi;
Msampha unatyoka ndi ife tinaonioka.
8 Thandizo lathu liri m’dzina la Yehova,
Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.