Pemphero la wonyozedwa
Nyimbo yokwerera.
1 Ndikweza maso anga kwa Inu,
Kwa Inu wakukhala kumwamba.
2 Taonani, monga maso a anyamata ayang’anira dzanja la ambuye ao,
Monga maso a adzakazi ayang’anira dzanja la mbuye wao wamkazi:
Momwemo maso athu ayang’anira Yehova Mulungu wathu,
Kufikira aticitira cifundo.
3 Muticitire cifundo, Yehova, muticitire cifundo;
Pakuti takhuta kwambiri ndi mnyozo.
4 Moyo wathu wakhuta ndithu
Ndi kuseka kwa iwo osasowa kanthu,
Ndi mnyozo wa odzikuza.