Masalmo 121

Mulungu Msungi wokhulupirika wa anthu ace

Nyimbo yokwerera.

1 Ndikweza maso anga kumapiri:

Thandizo langa lidzera kuti?

2 Thandizo langa lidzera kwa Yehova,

Wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.

3 Sadzalola phazi lako literereke:

Iye amene akusunga sadzaodzera.

4 Taonani, wakusunga Israyea

Sadzaodzera kapena kugona.

5 Yehova ndiye wakukusunga;

Yehova ndiye mthunzi wako wa ku dzanja lako lamanja.

6 Dzuwa silidzawamba usana,

Mwezi sudzakupanda usiku.

7 Yehova adzakusunga kukucotsera zoipa ziri zonse;

Adzasunga moyo wako.

8 Yehova adzasungira kuturuka kwako ndi kulowa kwako,

Kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.