Mulungu ndi wa ulemerero, mafano ndiwo acale
1 Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, Koma kwa dzina lanu patsani ulemerero,
Cifukwa ca cifundo canu, ndi coonadi canu.
2 Aneneranji amitundu,
Ali kuti Mulungu wao?
3 Koma Mulungu wathu ndiye ali m’mwamba;
Acita ciri conse cimkonda.
4 Mafano ao ndiwo a siliva ndi golidi,
Nchito za manja a anthu.
5 Pakamwa ali napo, koma osalankhula;
Maso ali nao, koma osapenya;
6 Makutu ali nao, koma osamva;
Mphuno ali nazo, koma osanunkhiza;
7 Manja ali nao, koma osagwira;
Mapazi ali nao, koma osayenda;
Kapena sanena pammero pao,
8 Adzafanana nao iwo akuwapanga;
Ndi onse akuwakhulupirira,
9 Israyeli, khulupirira Yehova:
Ndiye mthandizi wao ndi cikopa cao.
10 Nyumba ya Aroni, khulupirira Yehova:
Ndiye mthandizi wao, ndi cikopa cao.
11 Inu akuopa Yehova, khulupirirani Yehova;
Ndiye mthandizi wao ndi cikopa cao.
12 Yehova watikumbukila; adzatidalitsa:
Adzadalitsa nyumba ya Israyeli;
Adzadalitsa nyumba ya Aroni.
13 Adzadalitsa iwo akuopa Yehova,
Ang’ono ndi akuru.
14 Yehova akuonjezereni dalitso, Inu ndi ana anu.
15 Odalitsika inu a kwa Yehova,
Wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.
16 Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova;
Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.
17 Akufa salemekeza Yehova,
Kapena ali yense wakutsikira kuli cete:
18 Koma ife tidzalemekeza Yehova
Kuyambira tsopano kufikira nthawi yonse.
Haleluya.