Ufumu wa Ambuye
Salmo la Davide,
1 Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani pa dzanja lamanja langa,
Kufikira nditaika adani anu copondapo mapazi anu.
2 Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kucokera ku Ziyoni;
Citani ufumu pakati pa adani anu.
3 Anthu anu adzadzipereka eni ace tsiku la camuna canu:
M’moyera mokometsetsa, mobadwira tnatanda kuca,
Muli nae mame a ubwana wanu.
4 Yehova walamulira, ndipo sadzasintha,
Inu ndinu wansembe kosatha
Monga mwa cilongosoko ca Melikizedeke.
5 Yehova pa dzanja lamanja lako
Adzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wace.
6 Adzaweruza mwa amitundu,
Adzadzaza dziko ndi mitembo;
Adzaphwanya mitu m’maiko ambiri.
7 Adzamwa ku mtsinje wa panjira;
Cifukwa cace adzaweramutsa mutu wace.