Masalmo 108

Davide ayimbira Mulungu womgonjetsera adani

Nyimbo. Salmo la Davide.

1 Wakhazikika mtima wanga, Mulungu;

Ndidzayimba, inde ndidzayimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga.

2 Galamukani, cisakasa ndi zeze;

Ndidzauka ndekha mamawa.

3 Ndidzakuyamikani mwa mitundu ya anthu, Yehova:

Ndipo ndidzayimba zakukulemekezani mwa anthu.

4 Pakuti cifundo canu ncacikuru kupitirira kumwamba,

Ndi coonadi canu kufikira mitambo.

5 Kwezekani pamwamba pa thambo, Mulungu;

Ndi ulemerero wanu pamwamba pa dziko lonse lapansi.

6 Kuti okondedwa anu alanditsidwe,

Pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutibvomereze.

7 Mulungu analankhula m’ciyero cace; ndidzakondwerera:

Ndidzagawa Sekemu; ndidzayesa muyeso cigwa ca Sukoti.

8 Gileadi ndi wanga: Manase ndi wanga;

Ndi Efraimu ndiye mphamvu ya mutu wanga;

Yuda ndiye wolamulira wanga.

9 Moabu ndiye mkhate wanga;

Pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga;

Ndidzapfuulira Filistiya,

10 Adzandifikitsa ndani m’mudzi wa m’linga?

Adzanditsogolera ndani ku Edomu?

11 Si ndinu Mulungu, amene mwatitaya

Osaturuka nao magulu athu?

12 Tithandizeni mumsauko;

Pakuti cipulumutso ca munthu ndi cabe.

13 Mwa Mulungu tidzacita molimbika mtima:

Ndipo Iye adzapondereza otisautsa.