Wopsinjika apempha Mulungu acitire anthu ace cifundo, amitundu nammverenso
Pemphero la Wozunzika, m’mene anakomoka natsanulira cobnaatira cace pamaso pa Yehova,
1 Yehova, imvani pemphero langa,
Ndipo mpfuu wanga ufikire Inu.
2 Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga;
Mundichereze khutu lanu;
Tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga,
3 Popeza masiku anga akanganuka ngati utsi,
Ndi mafupa anga anyeka ngati nkhuni.
4 Mtima wanga ukunga udzu wamweta, nufota;
Popeza ndiiwala kudya mkate wanga.
5 Cifukwa ca liu la kubuula kwanga
Mnofu wanga umamatika ku mafupa anga.
6 Ndikunga bvuwo m’cipululu;
Ndikhala ngati kadzidzi wa kumabwinja.
7 Ndidikira, ndikhala ngati mbawa
Iri yokha pamwamba pa tsindwi.
8 Adani anga anditonza tsiku lonse;
Akundiyarukirawo alumbirira ine.
9 Pakuti ndadya mapulusa ngati mkate,
Ndi kusanganiza-comwera canga ndi misozi,
10 Cifukwa ca ukali wanu ndi kuzaza kwanu;
Popeza munandinyamula ndipo munandigwetsa.
11 Masiku anga akunga mthunzi womka m’tali;
Ndipo ine ndauma ngati udzu.
12 Koma Inu, Yehova, mukhalabe ku nthawi yonse;
Ndi cikumbukilo canu ku mibadwo mibadwo.
13 Inu mudzauka, ndi kucitira nsoni Ziyoni;
Popeza yafika nyengo yakumcitira cifundo, nyengo yoikika.
14 Pakuti atumiki anu akondwera nayo miyala yace,
Nacitira cifundo pfumbi lace.
15 Pamenepo amitundu adzaopa dzina la Yehova,
Ndi mafumu onse a dziko lapansi ulemerero wanu;
16 Pakuti Yehova anamanga Ziyoni,
Anaoneka m’ulemerero wace;
17 Anasamalira pemphero la iwo akusowa konse,
Osapepula pemphero lao.
18 Ici adzacilembera mbadwo ukudza;
Ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova.
19 Pakuti anapenya pansi ali kumwamba kuli malo ace opatulika;
Yehova pokhala kumwamba anapenya dziko lapansi;
20 Kuti amve kubuula kwa wandende;
Namasule ana a imfa,
21 Kuti anthu alalikire dzina la Yehova m’Ziyoni,
Ndi cilemekezo cace m’Yerusalemu;
22 Posonkhana pamodzi mitundu ya anthu,
Ndi maufumu kuti atumikire Yehova.
23 Iye analanda mphamvu yanga panjira;
Anacepsa masiku anga.
24 Ndinati, Mulungu wanga, musandicotse pakati pa masiku anga:
Zaka zanu zikhalira m’mibadwo mibadwo.
25 Munakhazika dziko lapansi kalelo;
Ndipo zakumwamba ndizo nchito ya manja anu.
26 Zidzatha izi, koma Inu mukhala:
Inde, zidzatha zonse ngati cabvala;
Mudzazisintha ngati maraya, ndipo zidzasinthika:
27 Koma Inu ndinu yemweyo,
Ndi zaka zanu sizifikira kutha.
28 Ana a atumiki anu adzakhalitsa,
Ndi mbeu zao zidzakhazikika pamaso panu.