Davide akuti adzasamala okhulupirika nadzacotsa oipa
Salmo la Davide.
1 Ndidzayimba za cifundo ndi ciweruzo;
Ndidzayimba zakukulemekezani Inu, Yehova.
2 Ndidzacita mwanzeru m’njira yangwiro;
Mudzandidzera liti?
Ndidzayenda m’nyumba mwanu ndi mtima wangwiro.
3 Sindidzaika cinthu coipa pamaso panga;
Cocita iwo akupatuka padera cindiipira;
Sicidzandimamatira.
4 Mtima wopulukira udzandicokera;
Sindidzadziwana naye woipa.
5 Wakuneneza mnzace m’tseri ndidzamdula;
Wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.
6 Maso anga ayang’ana okhulupirika m’dziko, kuti akhale ndi Ine;
Iye amene ayenda m’njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.
7 Wakucita cinyengo sadzakhala m’kati mwa nyumba yanga;
Wakunena mabodza sadzakhazikika pamaso panga.
8 Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m’dziko;
Kuduliratu onse akucita zopanda pace ku mudzi wa Yehova.