Athamangira Mulungu pothawa adani omtsata
1 Muimiranji patari, Yehova?
Mubisaliranji m’nyengo za nsautso?
2 Podzikuza woipa apsereza waumphawi;
Agwe m’ciwembu anapanganaco.
3 Pakuti woipa adzitamira cifuniro ca moyo wace,
Adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.
4 Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yace, akuti, Sadzafunsira.
Malingaliro ace onse akuti, Palibe Mulungu.
5 Mayendedwe ace alimbika nthawi zonse;
Maweruzo anu ali pamwamba posaona iye;
Adani ace onse awanyodola.
6 Ati mumtima mwace, Sindidzagwedezeka ine;
Ku mibadwo mibadwo osagwa m’tsoka ine.
7 M’kamwa mwace mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kucenjerera;
Pansi pa lilime lace pali cibvutitso copanda pace.
8 Akhala m’molalira midzi;
Mobisalamo akupha munthu wosacimwa:
Ambisira waumphawi nkhope yace,
9 Alalira monga mkango m’ngaka mwace;
Alalira kugwira wozunzika:
Agwira wozunzika, pakumkola m’ukonde mwace.
10 Aunthama, nawerama,
Ndipo aumphawi agwa m’zala zace.
11 Anena m’mtima mwace, Mulungu waiwala;
Wabisa nkhope yace; sapenya nthawi zonse,
12 Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu;
Musaiwale ozunzika.
13 Woipa anyozeranii Mulungu,
Anena m’mtima mwace, Simudzafunsira?
14 Mwapenya; pakuti mumayang’anira cibvutitso ndi cisoni kuti acipereke m’manja mwanu;
Waumphawi adzipereka kwa Inu;
Wamasiye mumakhala mthandizi wace.
15 Thyolani mkono wa woipa;
Ndipo wocimwa, mutsate coipa cace kufikira simucipezanso cina.
16 Yehova ndiye Mfumu ku nthawi yamuyaya;
Aonongeka amitundu m’dziko lace.
17 Yehova, mwamva cikhumbo ca ozunzika:
Mudzakhazikitsa mtima wao, mudzachereza khutu lanu:
18 Kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi,
Kuti munthu wa pa dziko lapansi angaonjeze kuopsa.