Hoseya 3

Akwatiranso mkazi woipa, kufaniziranso zocita ana a Israyeli

1 Ndipo Yehova anati kwa ine, Mukanso, konda mkazi wokondedwa ndi bwenzi lace, koma wakucita cigololo monga Yehova akonda ana a Israyeli, angakhale atembenukira ku milungu yina, nakonda ncinci za mphesa zouma.

2 M’mwemo ndinadzigulira iye ndi ndalama khumi ndi zisanu zasiliva, ndi homeri ndi nusu wa barele;

3 ndipo ndinati kwa iye, Uzikhala ndi ine masiku ambiri, usacita cigololo, usakhala mkazi wa mwamuna ali yense; momwemo inenso nawe.

4 Pakuti ana Israyeli adzakhala masiku ambiri a opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda coimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;

5 atatero ana a Israyeli adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku ukoma wace masiku otsiriza.