Cibvumbulutso 15

Angelo asanu ndi awiri ndi miliri isanu ndi iwiri

1 Ndipo ndinaona cizindikilo cina m’mwamba, cacikuru ndi cozizwitsa, angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, ndiyo yotsiriza, kuti mwa iyo watsirizika mkwiyo wa Mulungu.

2 Ndipo ndinaona ngati nyanja yamandala yosanganiza ndi moto; ndipo iwo amene anaeilaka ciromboco, ndi fano lace ndi ciwerengero ca dzina lace, anaimirira pa nyanja ya mandala, nakhala nao azeze a Mulungu.

3 Ndipo ayimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Nchito zanu nzazikuru ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.

4 Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Cifukwa Inu nokha muli woyera; cifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.

5 Ndipo zitatha izi ndinaona, ndipo panatseguka pa Kacisi wa cihema ca umboni m’Mwamba:

6 Ndipo anaturuka m’Kacisi angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, atabvala mwala woyera, ndi wonyezimira, namangira malamba agolidi pacifuwa pao,

7 Ndipo cimodzi ca zamoyo zinai cinapatsa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zagolidi zodzala ndi mkwiyo wa Mulungu wakukhala ndi moyo ku nthawi za nthawi.

8 Ndipo Kacisi anadzazidwa ndi utsi wocokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu yace; ndipo palibe munthu anakhoza kulowa m’Kacisi kufikira ikatha miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri.