Nyimbo yoyamikira ya Davide
1 Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m’dzanja la adani ace onse, ndi m’dzanja la Sauli.
2 Ndipo anati:-
Yehova ndiye thanthwe langa, ndi ngaka yanga, ndi mpulumutsi wanga, wangadi;
3 Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzamkhulupirira;
Cikopa canga, ndi nyanga ya cipulumutso canga, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga;
Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuciwawa.
4 Ndidzaitanakwa Yehovaamene ayenera timtamande;
Comweco ndidzapulumutsidwa kwa adani anga.
5 Pakuti mafunde a imfa anandizinga,
Mitsinje ya zopanda pace inandiopsa ine.
6 Zingwe za kumanda zinandizingira;
Misampha ya imfa inandifikira ine.
7 M’kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova,
Inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga;
Ndipo Iye anamva mau anga ali m’kacisi wace,
Ndi kulira kwanga kunafika ku makutuace.
8 Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira.
Maziko a dziko la kumwamba anasunthika
Nagwedezeka, cifukwa iye anakwiya.
9 M’mphuno mwace munaturuka utsi,
Ndi moto woturuka m’kamwa mwace unaononga;
Makala anayaka nao.
10 Anaweramitsa miyambanso, natsika;
Ndipo mdima wandiwe-yani unali pansi pa mapazi ace.
11 Ndipo iye anaberekeka pa Kerubi nauluka;
Inde anaoneka pa mapiko a mphepo,
12 Ndipo anayesa mdimawo ngati mahema omzungulira iye,
Kusonkhana kwa madzi ndi mitambo yocindikira ya mlengalenga.
13 Ceza ca pamaso pace
Makala a mota anayaka,
14 Yehova anagunda kumwamba;
Ndipo Wam’mwambamwamba ananena mau ace.
15 Ndipo iye anatumiza mibvi, nawawaza;
Mphezi, nawaopsa,
16 Pamenepo m’munsi mwa nyanja munaoneka,
Maziko a dziko anaonekera poyera,
Ndi mthonzo wa Yehova,
Ndi mpumo wa mweya wa m’mphuno mwace.
17 Iye anatumiza kucokera kumwamba nanditenga;
Iye ananditurutsa m’madzi akuru;
18 Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,
Kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu,
19 Anandifikira ine tsiku la tsoka langa;
Koma Yehova anali mcirikizo wanga,
20 Iye ananditurutsanso ku malo akuru;
Iye anandipulumutsa, cifukwa akondwera ndi ine.
21 Yehova anandibwezera monga mwa colungama canga;
Monga mwa kuvera kwa manja anga anandipatsa mphotho.
22 Pakuti ndinasunga njira za Yehova,
Osapambukira koipa kusiya Mulungu wanga.
23 Pakuti maweruzo ace onse anali pamaso panga;
Ndipo za malemba ace, sindinawapambukira.
24 Ndinakhalanso wangwiro kwa iye,
Ndipo ndinadzisunga kusacita kuipa kwanga.
25 Cifukwa cace Yehova anandibwezera monga mwa colungama canga;
Monga mwa kuyera kwanga pamaso pace.
26 Ndi acifundo Inu mudzadzionetsa wacifundo,
Ndi munthu wangwiro mudzadzionetsa wangwiro;
27 Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima;
Ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza.
28 Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa;
Koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwacepetse.
29 Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova;
Ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga.
30 Pakuti ndi Inu ndithamangira gulu;
Ndi Mulungu wanga ndilumphira linga.
31 Kunena za Mulungu, njira yace iri yangwiro;
Mau a Yehova anayesedwa; iye ndiye cikopa kwa onse akukhulupirira iye.
32 Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova?
Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu?
33 Mulungu ndiye Gnga langa lamphamvu;
Ndipo iye ayendetsa angwiro mu njira yace.
34 Iye asandutsa mapazi ace akunga mapazi a mbawala;
Nandiika pa misanje yanga.
35 Iye aphunzitsa manja anga nkhondo;
Kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa.
36 Ndiponso munandipatsa cikopa ca cipulumutso canu;
Ndi kufatsa kwanu kunandikulitsa.
37 Munakulitsa kulunza kwanga pansi panga,
Ndi mapazi anga sanaterereka.
38 Ndinapitikitsa adani anga, ndi kuwaononga;
Ndiponso sindinabwerera mpaka nditawatha.
39 Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sakhoza kuuka,
Inde anagwa pansi pa mapazi anga.
40 Pakuti Inu munandimanga m’cuuno ndi mphamvu ya kunkhondo; Munandigonjetsera akundiukira.
41 Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo,
Kuti ndiwalikhe akudana ndi ine.
42 Anayang’ana iwo, koma panalibe wopulumutsa;
Ngakhale kwa Yehova, koma iye sanawayankha.
43 Pomwepo ndinawasansantha asalale ngati pfumbi la padziko,
Ndinawapondereza ngati dothi la m’makwalala.
44 Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga;
Munandisunga ndikhale mutu wa amitundu;
Anthu amene sindinawadziwa adzanditsumikira ine.
45 Alendo adzandigonjera ine,
Pakumva za ine, adzandimbera pomwepo.
46 Alendo adzafota,
Nadzabwera ndi kunthunthumira oturuka mokwiririka mwao.
47 Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;
Ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la cipulumutso canga;
48 Inde Mulungu wakundibwezera cilango ine,
Ndi kundigonjetsera anthu a mitundu.
49 Amene anditurutsa kwa adani anga;
Inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira;
Mundipulumutsa kwa munthu waciwawa.
50 Cifukwa cace ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu,
Ndipo ndidzayimba zolemekeza dzina lanu.
51 Iye apatsa mfumu yace cipulumutso cacikuru;
Naonetsera cifundo wodzozedwa wace,
Kwa Davide ndi mbeu yace ku nthawi zonse.