2 Mbiri 27

Yotamu mfumu ya Yuda

1 Yotamu anali wa zaka makumi awiri, mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m’Yerusalemu zaka khumi ndi zisanu ndi cimodzi; ndi dzina la mace ndiye Yerusa mwana wa Zadoki.

2 Ndipo anacita zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo adacitira atate wace Uziya; pokhapo sanalowa m’Kacisi wa Yehova. Koma anthu anacitabe zobvunda.

3 Anamanga cipata ca kumtunda ca nyumba ya Yehova, ndi pa linga la Ofeli anamanga kwakukuru.

4 Namanga midzi m’mapiri a Yuda, ndi m’nkhalango anamanga nyumba zansanja, ndi nsanja zomwe.

5 Anayambananso ndi mfumu ya ana a Amoni, namgonjetsa, Ndi ana a Amoni anamninkha caka comweci matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zikwi khumi, ndi ya barele zikwi khumi. Ana a Amoni anabwera nazo zomwezo kwa iye caka caciwiri ndi cacitatu comwe.

6 Momwemo Yotamu anakula mphamvu, popeza anakonza njira zace pamaso pa Yehova Mulungu wace.

7 Macitidwe ena tsono a Yotamu, ndi nkhondo zace zonse, ndi njira zace, taonani, zalembedwa m’buku la mafumu a Israyeli ndi Yuda.

8 Anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m’Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi.

9 Ndipo Yotamu anagona ndi makolo ace, namuika m’mudzi wa Davide; ndi Ahazi mwana wace anakhala mfumu m’malo mwace.